Masalmo 87:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndidzachula Rahabu ndi Babulo kwa iwo ondidziwa Ine;Taonani, Filistiya ndi Turo pamodzi ndi Kusi;Uyu anabadwa komweko.

5. Ndipo adzanena za Ziyoni,Uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo;Ndipo Wam'mwambamwamba ndiye aclzaukhazikitsa.

6. Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu.Uyu anabadwa komweko.

7. Ndipo oyimba ndi oomba omwe adzati,Akasupe ansa onse ali mwa inu.

Masalmo 87