15. Cigumula cisandifotsere,Ndipo cakuya cisandimize;Ndipo asanditsekere pakamwa pace pa dzenje.
16. Mundiyankhe Yehova; pakuti cifundo canu ncokoma;Munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
17. Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;Pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.
18. Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;Ndipulumutseni cifukwa ca adani anga,
19. Mudziwa cotonza canga, ndi manyazi anga, ndi cimpepulo canga:Akundisautsa ali pamaso panu,
20. Cotonza candiswera mtima, ndipo ndidwala ine;Ndipo ndinayembekeza wina wondicitira cifundo, koma palibe;Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
21. Ndipo anandipatsa ndulu ikhale cakudya canga;Nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
22. Gome lao likhale msampha pamaso pao;Pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.
23. M'maso mwao mude, kuti asapenye;Ndipo munjenjemeretse m'cuuno mwao kosalekeza.