7. Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha;Maso ace ayang'anira amitundu;Opikisana ndi Iye asadzikuze.
8. Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace:
9. Iye amene asunga moyo wathu tingafe,Osalola phazi lathu literereke.
10. Pakati munatiyesera, Mulungu:Munatiyenga monga ayenga siliya.
11. Munapita nafe kuukonde;Munatisenza cothodwetsa pamsana pathu.
12. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa.
13. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,Ndidzakucitirani zowinda zanga,
14. Zimene inazichula milomo yanga,Ndinazinena pakamwa panga pasautsika ine.