Masalmo 64:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma Mulungu adzawaponyera mubvi;Adzalaswa modzidzimutsa,

8. Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;Onse akuwaona adzawathawa.

9. Ndipo anthu onse adzacita mantha;Nadzabukitsa cocita Mulungu,Nadzasamalira nchito yace.

10. Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye;Ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.

Masalmo 64