Masalmo 63:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7. Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8. Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9. Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.

Masalmo 63