Masalmo 54:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.

2. Imvani pemphero langa, Mulungu;Cherani khutu mau a pakamwa panga.

3. Pakuti alendo andiukira,Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;Sadziikira Mulungu pamaso pao.

Masalmo 54