Masalmo 52:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo olungama adzaciona, nadzaopa,Nadzamseka, ndi kuti,

7. Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyesa Mulungu mphamvu yace;Amene anatama kucuruka kwa cuma cace,Nadzilimbitsa m'kuipsa kwace.

8. Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi waazitona m'nyumba ya Mulungu:Ndikhulupirira cifundo ca Mulungu ku nthawi za nthawi.

9. Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munacicita ici:Ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ici ncokoma, pamaso pa okondedwa anu,

Masalmo 52