Masalmo 52:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Udzitamandiranji ndi coipa, ciphonaiwe?Cifundo ca Mulungu cikhala tsiku lonse.

2. Lilime lako likupanga zoipa;Likunga lumo lakuthwa, lakucita monyenga.

3. Ukonda coipa koposa cokoma;Ndi bodza koposa kunena cilungamo.

4. Ukonda mau onse akuononga, Lilime lacinyengo, iwe.

5. Potero Mulungu adzakupasula ku nthawi zonse,Adzakucotsa nadzakukwatula m'hema mwako,Nadzakuzula, kukucotsa m'dziko la amoyo.

Masalmo 52