Masalmo 51:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mundilengere mtima woyera, Mulungu;Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

11. Musanditaye kundicotsa pamaso panu;Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.

12. Mundibwezere cimwemwe ca cipulumutso canu;Ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

13. Pomwepo ndidzalangiza ocimwa njira zanu;Ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.

14. Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu,Ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;Lilime langalidzakweza Nyimbo ya cilungamo canu.

15. Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;Ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.

16. Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;Nsembe yopsereza simuikonda.

17. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

18. Citirani Ziyoni cokoma monga mwa kukondwera kwanu;Mumange malinga a miyala a Yerusalemu.

Masalmo 51