Masalmo 49:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Usaope polemezedwa munthu,Pocuruka ulemu wa nyumba yace;

17. Pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kali konse;Ulemu wace sutsika naye kumtsata m'mbuyo.

18. Angakhale anadalitsa moyo wace pokhala ndi moyo,Ndipo anthu akulemekeza iwe, podzicitira wekha zokoma,

19. Adzamuka ku mbadwo wa makolo ace;Sadzaona kuunika nthawi zonse.

20. Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,Afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo.

Masalmo 49