Masalmo 47:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;Ndiye mfumu yaikuru pa dziko lonse lapansi.

3. Atigonjetsera anthu,Naika amitundu pansi pa mapazi athu.

4. Atisankhira colowa cathu,Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.

5. Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.

6. Yimbirani Mulungu, yimbirani;Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.

Masalmo 47