Masalmo 44:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cifukwa ca mau a wotonza wocitira mwano;Cifukwa ca mdani ndi wobwezera cilango,

17. Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,Ndipo sitinacita monyenga m'pangano lanu.

18. Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo,Ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;

19. Mungakhale munatityola mokhala zirombo,Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.

Masalmo 44