Masalmo 44:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Mugulitsa anthu anu kwacabe,Ndipo mtengo wace simupindula nao.

13. Mutisandutsa cotonza kwa anzathu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga.

14. Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,Ndi kuti anthu atipukusire mitu.

15. Tsiku lonse cimpepulo canga cikhala pamaso panga,Ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.

Masalmo 44