Masalmo 39:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.

6. Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:Indedi abvutika cabe:Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?

7. Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani?Ciyembekezo canga ciri pa Inu.

8. Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse:Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa.

9. Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga;Cifukwa inu mudacicita.

10. Mundicotsere cobvutitsa canu;Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu.

11. Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu,Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce:Indedi, munthu ali yense ali cabe.

Masalmo 39