Masalmo 35:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Gwirani cikopa cocinjiriza, Ukani kundithandiza.

3. Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola:Nenani ndi moyo wanga, Cipulumutso cako ndine.

4. Athe nzeru nacite manyazi iwo akufuna moyo wanga:Abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira ciwembu.

5. Akhale monga mungu kumphepo,Ndipo mngelo wa Yehova awapitikitse.

6. Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera,Ndipo mngelo wa Yehova awalondole.

7. Pakuti anandichera ukonde wao m'mbunamo kopanda cifukwa,Anakumbira moyo wanga dzenje kopanda cifukwa.

8. Cimgwere modzidzimutsa cionongeko;Ndipo ukonde wace umene anaucha umkole yekha mwini:Agwemo, naonongeke m'mwemo.

Masalmo 35