Masalmo 35:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakati pa onyodola pamadyerero,Anandikukutira mano.

17. Ambuye, mudzapenyerabe nthawi yanji?Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,Wanga wa wokha kwa misona ya mkango.

18. Ndidzakuyamikanimumsonkhano waukuru:M'cikhamu ca anthu ndidzakulemekezani.

19. Adani anga asandikondwerere ine monyenga;Okwiya nane kopanda cifukwa asanditsinzinire.

Masalmo 35