Masalmo 34:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9. Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10. Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11. Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12. Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?

Masalmo 34