16. Palibe mfumu yoti gulu lalikuru limpulumutsa:Mphamvu yaikuru siicilanditsa ciphona,
17. Kavalo safikana kupulumuka naye:Cinkana mphamvu yace njaikuru sapulumutsa.
18. Taonani, diso la Yehova liri pa iwo akumuopa Iye,Pa iwo akuyembekeza cifundo cace;
19. Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,Ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.
20. Moyo wathu walindira Yehova:Iye ndiye thandizo lathu ndi cikopa cathu.