Masalmo 27:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,

4. Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.

5. Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.

6. Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga;Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera;Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.

7. Imvani, Yehova, liu langa popfuula ine:Mundicitirenso cifundo ndipo mundibvomereze.

8. Pamene munati, Punani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu:Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.

9. Musandibisire ine nkhope yanu;Musacotse kapolo wanu ndi kukwiya:Inu munakhala thandizo langa;Musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa cipulumutso canga,

10. Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,Koma Yehova anditola.

Masalmo 27