Masalmo 26:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;Kapena kutsagana nao anthu otyasika.

5. Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.

6. Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:

7. Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.

Masalmo 26