1. Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova.
2. Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu,Ndisacite manyazi;Adani anga asandiseke ine.
3. Inde, onse akuyembekezera Inu sadzacita manyaziAdzacita manyazi iwo amene acita monyenga kopanda cifukwa.
4. Mundidziwitse njira zanu, Yehova;Mundiphunzitse mayendedwe anu.