Masalmo 22:10-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cibadwire ine anandisiyira Inu:Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.

11. Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi:Pakuti palibe mthandizi.

12. Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga:Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,

13. Andiyasamira m'kamwa mwao,Ngati mkango wozomola ndi wobangula.

14. Ndathiridwa pansi monga madzi,Ndipo mafupa anga onse anaguluka:Mtima wanga ukunga sera; Wasungunuka m'kati mwa matumbo anga,

15. Mphamvu yanga yauma ngati phale;Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga;Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.

16. Pakuti andizinga agaru:Msonkhano wa oipa wanditsekereza;Andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.

17. Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse;Iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine:

18. Agawana zobvala zanga,Nalota maere pa malaya anga,

19. Koma Inu, Yehova, musakhale kutari;Mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.

20. Landitsani moyo wanga kulupanga;Wokondedwa wanga ku mphamvu ya garu,

21. Ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango;Inde mwandiyankha ine ndiri pa nyanga za njati,

22. Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga:Pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.

23. Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;Inu nonse mbumba ya Yakobo, mumcitire ulemu;Ndipo mucite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israyeli.

Masalmo 22