Masalmo 149:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,Ndi lupanga lakuthwa konse konse m'dzanja lao;

7. Kubwezera cilango akunja,Ndi kulanga mitundu ya anthu;

8. Kumanga mafumu ao ndi maunyolo,Ndi omveka ao ndi majerejede acitsulo;

9. Kuwacitira ciweruzo colembedwaco:Ulemu wa okondedwa ace onse ndi uwu.Haleluya.

Masalmo 149