Masalmo 148:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Anyamata ndiponso anamwali;Okalamba pamodzi ndi ana:

13. Alemekeze dzina la Yehova;Pakuti dzina lace lokha ndi lokwezeka;Ulemerero wace uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.

14. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ace,Cilemekezo ca okondedwa ace onse;Ndiwo ana a Israyeli, anthu a pafupi pa Iye,Haleluya,

Masalmo 148