Masalmo 148:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Haleluya.Lemekezani Yehova kocokera kumwamba;Mlemekezeni m'misanje.

2. Mlemekezeni, angelo ace onse;Mlemekezeni, makamu ace onse.

3. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira.

4. Mlemekezeni, m'mwambamwamba,Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.

5. Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.

Masalmo 148