8. Amene pakamwa pao alankhula zacabe,Ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lacinyengo.
9. Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;Pa cisakasa ca zingwe khumi ndidzayimbira zakukulemekezani.
10. Ndiye amene apatsa mafumu cipulumutso:Amene alanditsa Davide mtumiki wace ku lupanga loipa.
11. Ndilanditseni ndi kundipulumutsa ku dzanja la alendo,Amene pakamwa pao alankhula zacabe,Ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lacinyengo.