Masalmo 143:10-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kucidikha.

11. Mundipatse moyo, Yehova, cifukwa ca dzina lanu;Mwa cilungamo canu muturutse moyo wanga m'nsautso.

12. Ndipo mwa cifundo canu mundidulire adani anga,Ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;Pakuti ine ndine mtumiki wanu.

Masalmo 143