Masalmo 119:96-103 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

96. Ndinapenya malekezero ace a ungwiro wonse;Koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.

97. Ha! Ndikondadi cilamulo canu;Ndilingiriramo ine tsiku lonse.

98. Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;Pakuti akhala nane cikhalire.

99. Ndiri nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;Pakuti ndilingalira mboni zanu.

100. Ndizindikira koposa okalambaPopeza ndinasunga malangizo anu.

101. Ndinaletsa mapazi anga njira iri yonse yoipa,Kuti ndisamalire mau anu.

102. Sindinapatukana nao maweruzo anu;Pakuti Inu munandiphunzitsa.

103. Mau anu azunadi powalawa ine!Koposa uci m'kamwa mwanga.

Masalmo 119