Masalmo 119:66-70 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

66. Mundiphunzitse cisiyanitso ndi nzeru;Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.

67. Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.

68. Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.

69. Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

70. Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.

Masalmo 119