30. Ndinasankha njira yokhulupirika;Ndinaika maweruzo anu pamaso, panga,
31. Ndimamatika nazo mboni zanu;Musandicititse manyazi, Yehova.
32. Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,Mutakulitsa mtima wanga.
33. Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;Ndidzaisunga kufikira kutha kwace.
34. Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;Ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
35. Mundiyendetse mopita malamulo anu;Pakuti ndikondwera m'menemo.
36. Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu,Si ku cisiriro ai.