24. Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa,Ndizo zondipangira nzeru.
25. Moyo wanga umamatika ndi pfumbi;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
26. Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:Mundiphunzitse malemba anu.
27. Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;Kuti ndilingalire zodabwiza zanu.
28. Moyo wanga wasungunuka ndi cisoni:Mundilimbitse monga mwa mau anu.