157. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwoambiri;Koma sindinapatukana nazo mboni zanu.
158. Ndinapenya ocita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;Popeza sasamalira mau anu.
159. Penyani kuti ndikonda malangizo anu;Mundipatse moyo, Yehova, monga mwa cifundo canu.
160. Ciwerengero ca mau anu ndico coonadi;Ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161. Nduna zinandilondola kopanda cifukwa;Koma mtima wanga ucita mantha nao mau anu.