Masalmo 119:137-156 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

137. Inu ndinu wolungama, Yehova,Ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

138. Mboni zanuzo mudazilamuliraZiri zolungama ndi zokhulupirika ndithu.

139. Cangu canga cinandithera,Popeza akundisautsa anaiwala mau anu.

140. Mau anu ngoyera ndithu;Ndi mtumiki wanu awakonda.

141. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;Koma sindiiwala malemba anu.

142. Cilungamo canu ndico cilungamo cosatha;Ndi cilamulo canu ndico coonadi.

143. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

144. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.

145. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.

146. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.

147. Ndinapfuula kusanace:Ndinayembekezera mau anu.

148. Maso anga anakumika malonda a usiku,Kuti ndilingirire mau anu.

149. Imvani liu langa monga mwa cifundo canu;Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

150. Otsata zaciwembu andiyandikira;Akhala kutali ndi cilamulo canu.

151. Inu muli pafupi, Yehova;Ndipo malamulo anu onse ndiwo coonadi,

152. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,Kuti munazikhazika kosatha,

153. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;Pakuti sindiiwala cilamulo canu.

154. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.

155. Cipulumutso citalikira oipa;Popeza safuna malemba anu.

156. Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova;Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.

Masalmo 119