Masalmo 119:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Inu ndinu wodala Yehova;Ndiphunzitseni malemba anu.

13. Ndinafotokozera ndi milomo yangaMaweruzo onse a pakamwa panu,

14. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,Koposa ndi cuma conse,

15. Ndidzalingirira pa malangizo anu,Ndi kupenyerera mayendedwe anu.

Masalmo 119