Masalmo 116:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo.

10. Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula;Ndinazunzika kwambiri.

11. Pofulumizidwa mtima ndinati ine,Anthu Onse nga mabodza.

12. Ndidzabwezera Yehova cianiCifukwa ca zokoma zace zonse anandicitira?

13. Ndidzanyamula cikho ca cipulumutso,Ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova,

14. Ndidzacitazowindazanga za kwa Yehova,Tsopano, pamaso pa anthu ace onse.

Masalmo 116