2. Aneneranji amitundu,Ali kuti Mulungu wao?
3. Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;Acita ciri conse cimkonda.
4. Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi,Nchito za manja a anthu.
5. Pakamwa ali napo, koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;
6. Makutu ali nao, koma osamva;Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;
7. Manja ali nao, koma osagwira;Mapazi ali nao, koma osayenda;Kapena sanena pammero pao,
8. Adzafanana nao iwo akuwapanga;Ndi onse akuwakhulupirira,