Masalmo 113:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Haleluya;Lemekezani, inu atumiki a Yehova;Lemekezani dzina la Yehova,

2. Lodala dzina la Yehova.Kuyambira tsopano kufikira kosatha.

3. Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwaceLilemekezedwe dzina la Yehova.

4. Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,Ulemerero wace pamwambamwamba.

5. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?Amene akhala pamwamba patali,

Masalmo 113