4. Yehova walamulira, ndipo sadzasintha,Inu ndinu wansembe kosathaMonga mwa cilongosoko ca Melikizedeke.
5. Yehova pa dzanja lamanja lakoAdzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wace.
6. Adzaweruza mwa amitundu,Adzadzaza dziko ndi mitembo;Adzaphwanya mitu m'maiko ambiri.
7. Adzamwa ku mtsinje wa panjira;Cifukwa cace adzaweramutsa mutu wace.