2. Adzafotokoza ndani nchito zamphamvu za Yehova,Adzamveketsa ndani cilemekezo cace conse?
3. Odala iwo amene asunga ciweruzo,Iye amene acita cilungamo nthawi zonse.
4. Mundikumbukile, Yehova, monga momwe mubvomerezana ndi anthu anu;Mundionetsa cipulumutso canu:
5. Kuti ndione cokomaco ca osankhika anu,Kuti ndikondwere naco cikondwerero ca anthu anu,Kuti ndidzitamandire pamodzi ndi colowa canu.
6. Talakwa pamodzi ndi makolo athu;Tacita mphulupulu, tacita coipa.
7. Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto;Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji;Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
8. Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace,Kuti adziwitse cimphamvu cace.