24. Ndipo anacurukitsatu mtundu wa anthu ace,Nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.
25. Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ace,Kuti acite monyenga ndi atumiki ace.
26. Anatuma Mose mtumiki wace, Ndi Aroni amene adamsankha.
27. Anaika pakati pao zizindikilo zace,Ndi zodabwiza m'dziko la Hamu.
28. Anatumiza mdima ndipo kunada;Ndipo sanapikisana nao mau ace.