Masalmo 104:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa,Kufikira malo mudawakonzeratu.

9. Munaika malire kuti asapitirireko;Kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

10. Atumiza akasupe alowe m'makwawa;Ayenda pakati pa mapiri:

11. Zimamwamo nyama zonse za kuthengo;Mbidzi zipherako ludzu lao.

12. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo,Zimayimba pakati pa mitawi.

13. Iye amwetsa mapiri mocokera m'zipinda zace:Dziko lakhuta zipatso za nchito zanu.

14. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe,Ndi zitsamba acite nazo munthu;Naturutse cakudya cocokera m'nthaka;

15. Ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,Ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yace,Ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

Masalmo 104