2. Lemekeza Yehova, moyo wanga,Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:
3. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;Naciritsa nthenda zako zonse;
4. Amene aombola moyo wako ungaonongeke;Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:
5. Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.