Masalmo 102:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa ca liu la kubuula kwangaMnofu wanga umamatika ku mafupa anga.

6. Ndikunga bvuwo m'cipululu;Ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.

7. Ndidikira, ndikhala ngati mbawaIri yokha pamwamba pa tsindwi.

8. Adani anga anditonza tsiku lonse;Akundiyarukirawo alumbirira ine.

9. Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,Ndi kusanganiza-comwera canga ndi misozi,

Masalmo 102