Masalmo 101:6-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

7. Wakucita cinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.

8. Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko;Kuduliratu onse akucita zopanda pace ku mudzi wa Yehova.

Masalmo 101