Marko 9:12-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa cabe?

13. Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamcitiranso ziri zonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.

14. Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikuru la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.

15. Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlankhula.

16. Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsa na nao ciani?

17. Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;

18. ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo acita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti auturutse; koma sanakhoza.

19. Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.

20. Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsya; ndipo anagwa pansi nabvimbvinika ndi kucita thobvu.

21. Ndipo Iye anafunsa atate wace, kuti, Cimeneci cinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Cidamyamba akali mwana.

22. Ndipo kawiri kawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kucita kanthu mtithandize, ndi kuticitira cifundo.

23. Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

24. Pomwepo atate wa mwana anapfuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.

25. Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lirikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, turuka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

26. Ndipo pamene unapfuula, numng'ambitsa, unaturuka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

27. Koma Yesu anamgwira dzanja lace, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

28. Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ace anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuuturutsa?

29. Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kuturuka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

30. Ndipo anacoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafuna kuti munthu adziwe.

31. Pakuti anaphunzitsa ophunzira ace, nanena nao, kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

32. Koma iwo sanazindikira mauwo, naopa kumfunsa.

Marko 9