3. Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
4. Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.
5. Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.
6. Ndipo anazizwa cifukwa ca kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.