Marko 3:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lace lopuwala.

2. Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamciritsa dzuwa la Sabata; kuti ammange mlandu.

3. Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.

4. Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.

5. Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva cisoni cifukwa ca kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linacira dzanja lace.

Marko 3