16. Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ocimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ace, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ocimwa.
17. Ndipo pamene Yesu anamva ici, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.
18. Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?
19. Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.
20. Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.
21. Palibe munthu asokerera cigamba ca nsaru yaiwisi pa copfunda cakale; pena cimene coti cidzakonza cizomolapo, catsopanoco cizomoka pa cakaleco, ndipo ciboo cikulapo.