36. Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundicotsere cikho ici; komatu si cimene ndifuna Ine, koma cimene mufuna Inu.
37. Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?
38. Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.
39. Ndipo anacokanso, napemphera, nanena mau omwewo.
40. Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwa comyankha Iye.
41. Ndipo anadza kacitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; cakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu ocimwa.
42. Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.
43. Ndipo pomwepo, Iye ali cilankhulire, anadza Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ocokera kwa ansembe akuru ndi alembi ndi akuru.
44. Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa cizindikilo, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye cisungire.
45. Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa.
46. Ndipo anamthira manja, namgwira.
47. Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lace, nakantha kapolo wace wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lace.
48. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba?
49. Masiku onse ndinali nanu m'Kacisi ndirikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ici cacitika kuti malembo akwanitsidwe.
50. Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.
51. Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atapfundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira;
52. koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamarisece.
53. Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi,
54. Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.
55. Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.
56. Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana.