21. Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Kristu ali pano; kapena, Onani, uko; musabvomereze;
22. pakuti adzauka Akristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzacita zizindikilo ndi zozizwitsa, kuti akasoceretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.
23. Koma yanganirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.
24. Koma m'masikuwo, citatha cisautso cimeneco, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwace,
25. ndi nyenyezi zidzagwa kucokera m'mwamba ndi mphamvu ziri m'mwamba zidzagwedezeka.